2021 MSCE Chichewa II Loyola

Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 10

EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

LOYOLA JESUIT SECONDARY SCHOOL

MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION MOCK EXAMINATION

CHICHEWA
SUBJECT NUMBER: M032/II
Time Allowed: 1hour 45 mins
PAPER II
(90 marks)
Malangizo:
1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi
Masamba osindikizidwa khumi. Question Tick Do not write in
Number questions if these columns
2. M’gawo A: Malamulo a chiyankhulo: answered
yankhani mafunso onse (maliksi 40
1

2
3. M’gawo B: kumvetsa nkhani : Yankhani
mafunso onse . (malikisi 20) 3

4. M’gawo C: Chifupikitso (Malikisi 15) 4

5
5. M’gawo D: Chimasuliro: (malikisi 15)
6
6. Lembani dzina lanu pamwamba pa t
7
Total
7. samba lililonse loyankhirapo.

8. Muchitebulo chili kumbalichi

Onetsetsani funso lililonse lomwe
mwayankha pochonga
mubokosi lomwe lili kutsogolo kwake.

9. Perekani pepalali kwa

oyagng’aninra mayeso
nthawi ikakwana.
© 2021 Loyola mock Turn over

Page 1 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

Gawo A (Malikisi 40)

Malamulo a Chiyankhulo

1 a. Perekani ntchito zomwe maina atsekedwa mzere kunsi kwawo akugwira m’ziganizo zotsatirazi:

i. Kamuzu adachokera ku Chiwengo

____________________________________________________________________

ii. A bungwe amugulira mtsogoleri galimoto

_______________________________________________________________________

iii. John Chilembwe, mbusa, adaimadi pachoona.

__________________________________________________________________

iv. Awa si makolo ake, wangotinamiza.

__________________________________________________________________

v. Ndibwera ndi mnzanga kuti mumudziwe.

__________________________________________________________________

(Malikisi 5)

b. Perekani mtundu wa kapandamneni yemwe walembedwa mzere kunsi kwake m'ziganizo zotsatirazi:

i. Ndikuonapo phunziro kuseri kwa nthabwalazi.

______________________________________________________________

ii. Tacheza mmawa onse podikira malipiro.

______________________________________________________________

iii. Kuvina kwachikunja sikufunika mtchalichi.

______________________________________________________________

iv. Galu wake wamaanga uja wasowera ku uzimba.

______________________________________________________________

v. Apatseni bota lopolalo chifukwa sakonda kumwa zotentha

______________________________________________________________

(Malikisi 5)

Page 2 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

2 a. Lembani chiganizo chimodzi pa mtundu wina uli wonse wa kanenendwe ka aneni walembedwa
m'munsimu:

i. Kanenendwe
kacholinga____________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________

ii. Kanenedwe kolamula molangiza kapena

kuchenjeza____________________________________________________________________
____________________________________________________________________________

iii. Kanenedwe kofunsa

_____________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________
(Malikisi 6)

b.Perekani ntchito zomwe aphatikiri omwe ali ndi mzere kunsi kwawo akugwira m’ziganizo
zotsatirazi:

i. Ife tilibe chonena. ________________________________________________________________

ii. Ndidya chakudya akabwera.

_____________________________________________________________________________

iii. Mnyamata uja wadziphadi.

_____________________________________________________________________________

iv. Tingakhute kansimaka?

_____________________________________________________________________________

(Malikisi 4)

3 a Pangani ziganizo zomveka bwino ndi zining’a zotsatirazi:

i khala lamoto
_____________________________________________________________________________________

ii. pezapamwala.

(Malikisi 2)

Page 3 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

b. Sinthani mikuluwiko yotsatirayi kuti ikhale zifanifani:

i. m’chiuno mwa mwana simufa nkhuku.

__________________________________________________________________

ii. Kalulu azingwa kukapsa.

__________________________________________________________________

iii. Tsiku limodzi siliwoza mbewa.

__________________________________________________________________

(Malikisi 6)

4 a. Tchulani mtundu komanso ntchito yomwe nthambi yosaima payokha yomwe ili ndi mzere kunsi
kwake ikugwira m’ziganizo zotsatirazi:

i. Anawauza zonse zomwe anamva.

_______________________________________________________________________________

ii. Si matenda a Covid awa ndi chimfine chabe.

_______________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________________

iii. Mwana wa asisi wolongolora uja walandira chipulumutso.

_______________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________________

(Malikisi 6)

b. Lembani ziganizo zokhala ndi mitundu ya alowammalo otsatirawa ndipo mulembe mzere kunsi
kwa mlowammaloyo:

i. Wotsimikiza
______________________________________________________________________________

ii. Wopatula (wapayekha)

______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________

iii. Wodzichitira
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________

(Malikisi 6)

Page 4 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

GAWO B (Malikisi 20)

Kumvetsa Nkhani ndi Kusanthula Chiyankhulo

Werengani nkhani ili m’munsiyi ndipo muyankhe mafunso otsatirawo:

Anthu onse pasiwa paja adali khumakhuma podziwa kuti tsikulo silitha bwino. Atsibweni a Ndagona
adaonetseratu kuti adali wokwiya kwambiri ndi khalidwe la mpongozi wawo. Anthuwo adali maso yuu
kunjira kudikirira Mfumu Zathaizi yomwe inabwera kudzaonerera mwambo wosudzula amake
Ndaipalero, mkazi wa Ndagona.

Pasiwa paja padalibe phokoso lililonse. Anthu ankangoyang’anizana. Amake Ndaipalero ndi ana awo
asanu adali khuma pafupi ndi khola la ngondolo. Kamodzikamodzi mayiyu ankamveka kufwenthera
kusonyeza chisoni chake komanso mantha pa zomwe amaganiza kuti zitha kuchitika patsikulo. Katundu
yense wa m’nyumba ya Ndagona adali ataikidwa pamodzi ndipo atamuwaza kale mankhwala, ati
kuchotsa mizimu yoipa, komanso kuti anthu athe kumugwiritsa ntchito popanda vuto lililonse. Amake
Ndaipalero sadaloredwe kugwira kanthu kalikonse ati kuopa kuti angasowetse katundu wina m’nyumba
muja. Mayiyu adatchuka ndi nkhanza kwa abale a Ndagona. Anthu akuchimuna ankati mtengwa wawo
sankakhala bwino ndi ana ochokera kuchimunako. Chitsanzo chachikulu pakati pawo ankati chidali
Chodziwadziwa, mwana wa Napichesi, mlongo wake wa malemu, amene adalekera sukulu panjira
atachokera kutawuni kumene ankakhala ndi banja la Ndagona.

Chodziwadziwa atabwera kumudzi adauza anthu kuti adachoka kutawuni kuja chifukwa amake
Ndaipalero ankamuzunza kwambiri. Kumudzi kuja anthu adakhulupirira zonena za mwanayu ndipo
adangoti adzaona pakuti amake Ndaipalero adawachenjerera pogona.

Anthu akumudziwo sadadziwe kuti chifukwa chenicheni chimene Chodziwadziwa adachokera kutawuni
chidali chakuti iye ankathawa apolisi. Chidachitika chidali chakuti, tsiku lina Chodziwadziwa ndi anzake
asanu adapita kukayenda ku masitolo kutauni kuja. Ali chiyendere, adakumana ndi ana a amwenye atatu
amene adali kudya zakudya zosiyanasiyana. Chidziwadziwa ndi anzake aja adalephera kuugwira mtima
ndipo adatsomphola zakudya zija n’kuvulaza mmodzi mwa ana a amwenyewo. Kholo la mwanayo
lidaimba lamya ku polisi ndipo posachedwa apolisi adali nyomi pambuyo pa tiakapsala tija. Mwayi wa
Chodziwadziwa udali woti sadagwidwe, anzake onse aja adawakwidzinga unyolo.

Usiku watsiku limenelo Chodziwadziwa adalongeza katundu wake natulukira pazenera, waubutsa wa
kumudzi. Atafunsidwa kumudzi chomwe adachokera kutawuni, iye adangotchula pavunda khola. Iye
adanama kuti wathawa amake Ndaipalero. Uku kudali kuyamba kwa chidani pakati pa mayiyu ndi
akuchimuna.

Mfumu Zathaizi idafika dzuwa likuswa mtengo. Iyo idabwera ndi nduna ziwiri. Mwachepa, imodzi mwa
ndunazi adapempha anthu kuti ayandikire kusiwa kuja kuti mwambo uyambe.

Mfunseni, nduna Yachiwiri, adayamba kuyankhula, “Mosataya nthawi tipemphe mkokowogona

wakuchimuna kuti usudzule amake Ndaipalero, zikomo”

Page 5 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

“Ife, mfumu, tilibe mtunda wautali.” Mwatipeza adafotokoza. “Titakhala pansi pamudzi pano tagwirizana
kuti amake Ndaipalero ndi ana awo abwerere kwawo pakuti mnzawo amene adawabweretsa kunoyo
watsamira mkono. Tiwasudzula ndi K50 iyi. Ndikatero ndaima. Mukafunsa za chuma cha Ndagona,
mayiyu ndi ana akewo satengapo kanthu. Iwowa zawo adadyeratu wathu ali moyo. Choncho, nyumba,
mipando, galimoto, ngondolo ndi zovala zonse titenga ife kuti nafe tizipukutira misozi.”

Mfumu zathaizi idachita ngati yadzidzimuka kutulo ndipo idaimirira mokwiya kwambiri, imvekere,
“Mwatipeza, khala chete ndipo khala pansi! Anthu adyera ndi oipa mtima ngati inu sindidawaone
chibadwire changa! Tangoonani mkazi ndi ana a Ndagona ali apowo. Mukwalnda chumachi, mukuganiza
kuti azikathandizika ndi chiyani? Malipiro a sukulu azikawatenga kuti? Kodi kumene Ndagona ndi mkazi
wake ankapeza chumachi mudaliko? Ndafunsa zonsezi chifukwa cha mtudzu womwe Mwatipeza
wayankhula apa. Ndikudziwa kuti pamudzi pano muli ndi mangawa ndi mayiyu chifukwa cha zomwe
adakuuzani Chodziwadziwa. Komatu leroleroli apolisi adali kunyumba kwanga ndipo andiuza chifukwa
chenicheni chimene nthyamba wanuyu adachokera kutawuni. Si chifukwa cha amake Ndaipalero ayi,
koma chifukwa cha magwiragwira a mwana wanuyu! ndiye ine mfumu Zathaizi, ndikuti chumachi ati
atenge ndi mayiyu ndi ana ake. Inu yanu ikhala nyumba yokhayi pakuti ili pamudzi panu. Ikadakhala
kwina akadaitenganso, koma ndaopa kuti mungawathyole makosi anawa. Igwani apa ndi…..”

Mfumu Zathaizi sidatsirize mawu ake, pakuti apolisi adangoti balamunthu kutulukira. Chodziwadziwa
adati ayesere kuthawa koma agalu apolisi adamuwakha. Manyazi, mantha ndi chisoni zidawagwira anthu
a pamudzi paja. Adayamba kuchoka mmodzimmodzi, mitu ili werawera, manja ali mkhosi.

5 Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m’ziganizo zomveka bwino

i. Kodi anthu amadikirira chiyani pasiwa paja?

__________________________________________________________________

(Malikisi 1)

ii. Padali ubale wanji pakati pa amake Ndaipalero ndi Napichesi?

_______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________

(Malikisi 1)

iii. Kodi amake Ndaipalero adali kuganiza kuti zinthu ziyenda bwanji patsikulo, malinga ndi momwe
zidalili?
_______________________________________________________________________________
____________________________________________________________________________

(Malikisi 2)

iv. Tsimikizani kuti anthu a m’nkhaniyi ankakhulupirira miyambo yamakolo.

_______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
Page 6 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

(Malikisi 2)

v. Perekani chifukwa chimodzi chomwe akuchimuna adadanirana ndi amake Ndaipalero

_______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________

(Malikisi 2)

vi. Tsimikizani, popereka mfundo ziwiri, kuti Chodziwadziwa adali ndi khalidwe loipa.
_______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________

(Malikisi 2)

vii. Tsimikizani kuti Mfumu Zathaizi idalibe psete poweruza milandu.

_______________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________________

(Malikisi 2)

viii. Pezani zining’a m’nkhaniyi zomwe matanthauzo ake ndi awa:

i) Paphweka _______________________________________________________________

ii) Mlesi __________________________________________________________________

iii) Lipirani _______________________________________________________________

(Malikisi 3)

ix. Tchulani zifukwa ziwiri zomwe Mfumu Zathaizi adapereka kuti ateteze katundu wa amake
Ndaipalero ndi ana awo.
_______________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________________

(Malikisi 2)

x. N’chifukwa ninji anthu adabalalika mwadzidzidzi pasiwa paja?

_______________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________________

(Malikisi 1)

xi. Tsimikizani mfundo ya kumva zam’maluwa malinga ndi nkhaniyi.

_______________________________________________________________________________
____________________________________________________________________ (Malikisi 2)

Page 7 of 10
EXAMINATION No: _____________________ CLASS: ______________

GAWO C (Malikisi 15)

Chifupikitso

6. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala. Ili ndi mawu 149 ndipo mufupikitse kuti ikhale ndi mawu
osachepera 47 koma asapitilire 57.

ANTHU OCHITA MALONDA

Anthu amachita malonda osiyanasiyana padziko pano. Pali malonda monga ogulitsira m’sitolo, ena
amayendayenda ndi katundu wawo kulondola ogula, ndiponso ena amangokhala m’mbali mwa njira
kapena msewu. Onsewa amayembekeza kutolera pakutha kwa tsiku lililonse.

Ochita malonda oyendayenda ndi katundu wawo ali ndi zipsinjo zawozawo. Iwo amadziwa masiku a
nsika ku malo osiyanasiyana. Choncho tsiku lililonse la malonda amakambirana, nakumbutsana ulendo
ukhale wakuti tsiku linalo. Vuto limodzi lomwe limawadetsa nkhawa yosaneneka ndi m’mene
adzayendere kukafika kumsika winawo makamaka kukakhala kutali. Nkhawa bii chifukwa cha mmene
adzanyamulire katundu monga mabelo a zovala, matumba a mtedza, chimanga, mbatata, mawere,
maungu ndi zipangizo zomangira nyumba monga zitseko ndi mazenera, zomwe zimangoti mbwee pa
msika.

Nthawi zina akakhala kuti alipo angapo ochita malonda ochokera dera loyandikana, ambiriwa
amagwirizana zosonkherana ndalama yolipira galimoto imodzi yomwe ingathe kuwanyamulira katundu
wawo kupita ku misika yosiyanasiyana yomwe iwo amakagulitsako malonda. Izi zimawathandizira
kulowetsa ndalama yochepa yotengera katundu wawo kupita naye ku malonda. Zimawathandizanso
kuyenda mwachangu kupita kumisikako kukachita malonda awo.

Page 8 of 10

Chimasuliro

(Malikisi 15)

7 Masulirani nkhani yotsatirayi m’Chichewa chomveka bwino.

Marriages are a common tradition world over. East, West, North and South, people get married every day.
When two young people decide to settle down together as a couple, culture always finds its way into the
whole process. It all starts with meeting the prospective parents from both sides then dowry issues arise.

Dowry is the type of payment that is given to the parents as a token of appreciation for raising their child
in a decent way. In Africa, it is common that the man’s side is the one that pays dowry to the lady’s
family. This starts at the time of introduction, when the man is visiting the lady’s uncle or clan to inform
them about his interest to marry their daughter. In other parts of the world, however, it is the lady’s family
that pays dowry to the man’s family. This is a common trend in the Eastern culture. It is believed that
despite being raised decently by his parents, the young man will now be endowed to the huge task of
looking after the woman all his life, therefore his family has to be paid off. Huge sums of money are
involved in the process. If the lady’s family fails to pay the dowry, the wedding does not take place
anymore.

_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________________

Page 9 of 10

__________________________________________________________________________________

MAFUNSO ATHERA PANO

Page 10 of 10

You might also like