Chichewa Galamal
Chichewa Galamal
MABUKU ………………………………………………………………………………………………………………………………… 64
Page 2 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 1 MITUNDU YA MAWU
MUTU 2 DZINA
Dzina ndi mawu omwe timagwiritsa ntchito poyitana kapena potchula chinthu kapena ganizo lililonse.
MITUNDU YA MAYINA
1. Dzina lamwinimwini
Ili ndi dzina la chinthu chapachokha (chosawanda).
Zitsanzo za mayina amwinimwini ndi monga mayina a anthu, mitundu kapena mafuko a anthu, misewu,
nyanja, mitsinje, maiko, maboma, midzi, malo, mizinda, mapiri, masiku, miyezi, Mulungu, zigwa, milatho,
Zitsanzo:
Maliya, Malawi, Dedza, Namalenga, Januwale, Chitonga, Lachitatu, Chikhristu, Linthipe.
Page 3 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Polemba mayinawa timayamba ndi lembo laling’ono, pokhapokha ngati mayinawo akuyamba chiganizo
kapena pamene ndi mitu monga mitu ya nyimbo, ndakatulo ndi nkhani ndiye tiwayambe ndi lembo
lalikulu.
Zitsanzo:
nkhuku, mnyamata, mpweya, nzeru, mwala, fisi, ludzu, msonkho, uchembere, chulu.
Zitsanzo:
nyesi, nthunzi, mtambo, liwu, fungo, chigumula, utsi, mdima, mpweya, mwala, nkhuku, mnyamata.
Zitsanzo:
nzeru, ufulu, maganizo, ubwezi, nsanje, changu, dumbo, mantha, chilungamo, nkhanza, mtendere, maloto
5. Dzina launyinji
Ili ndi dzina la zinthu zowanda zomwe zili pagulu lawo la zinthu zofanana.
Zitsanzo:
msonkhano, mzukutu, mtolo, mulu, khwimbi, phava, bere, mpukutu, chipani, bungwe, gulu, mdipiti.
6. Dzina lachibale
Dzina lachibale (dzina lamphukira) ndi limodzi mwa mayina ambiri opangidwa kuchokera ku muzu kapena
tsinde limodzi la mawu.
Page 4 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Mayinawa amaimira maganizo osiyana kapena zinthu zosiyana ngakhale kuti kholo lawo (muzu kapena
Zitsanzo:
Tsinde Mayina achibale
tuma mtumwi
yenda ulendo
nthumwi
mlendo
mwendo ntumiki
utumiki
taya nthayo
lima ndime
mtaya
dima
mataya
chitayo mlimi
ulimi
NTCHITO ZA MAYINA
i) Kukhala mwininkhani (mchitantchito)
Zitsanzo:
Yohane wapita kumunda.
Chiponde chadyedwa ndi mzungu.
Zitsanzo:
Njoka yagwira chule.
Nazunga wandilembera kalata.
Page 5 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
v) Kukhala dzina loyitanira
Zitsanzo:
Yohane thawa njokayo.
Tabwera kuno, Manase.
MAGULU A MAYINA
Mayina amayikidwa m’magulu osiyanasiyana.
Tingazindikire gulu la dzina pogwiritsa ntchito mphatikiram’mbuyo wosonyeza zambiri komanso
pogwiritsa ntchito agwirizanitsi osonyeza chimodzi ndi zambiri.
Gulu (Mu –, A –)
Ili ndi gulu la mayina onse omwe amachulukitsidwa ndi mphatikiram’mbuyo ‘a–’.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
munthu anthu
m’bale abale
fisi afisi
mwamuna amuna
mzamba azamba
Page 6 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Gulu (Mu –, Mi –)
Ili ndi gulu la mayina onse kawirikawiri amachulukitsidwa ndi mphatikiram’mbuyo ‘mi–’.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
mulungu milungu
mkeka mikeka
muzu
mizu
mwambi miyambi
Gulu (U –, Ma –)
Ili ndi gulu la mayina onse omwe amayamba ndi lembo la liwu ‘u–’.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
udindo maudindo
uta mauta
udzudzu udzudzu
ufa ufa
Gulu (I –, Zi –)
Ili ndi gulu la mayina onse omwe timawaloza ndi iyi m’chimodzi ndipo m’zambiri timawaloza ndi izi.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
mimba mimba
mphwemphwa mphwemphwa
mfumu mfumu
inswa inswa
ndolo ndolo
Page 7 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Gulu (Chi –, Zi –)
Ili ndi gulu la mayina omwe amayamba ndi ch m’chimodzi ndipo amayamba ndi z m’zambiri.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
chambo zambo
chulu zulu
chikho zikho
chodyera zodyera
chibwana zibwana
Gulu (Li –, Ma –)
Ili ndi gulu la mayina omwe amayamba ndi ‘ma’ m’zambiri, ngakhale ena satero. Agwirizanitsi awo ndi i-
(m’chimodzi) ndi a- (m’zambiri).
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
bala mabala
khasu makasu
fupa mafupa
tsiku
masiku
diso
maso
Gulu (Ka –, Ti –)
Ili ndi gulu la mayina omwe amayamba ndi ‘ka’ m’chimodzi ndipo m’zambiri amayamba ndi ‘ti’.
Zitsanzo:
Chimodzi Zambiri
kamwana tiana
kanthu tinthu
kadiso timaso
Page 8 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Gulu (ku ndi tsinde la mneni)
Ili ndi gulu la mayina omwe amapangidwa pophatikiza ku- ku tsinde la mneni.
Zitsanzo:
kusaka (ku- ku saka)
kulemba (ku- ku lemba)
kugona (ku- ku gona)
patchire
m’mudzi
KAPANGIDWE KA MAYINA
Mayina amapangidwa m’njira zambiri monga:
-kulu ukulu
-ng’ono ung’ono
Page 9 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Mayina opanga kuchokera ku aonjezi
Chitsanzo
Muonjezi Dzina
bwino ubwino
lima mlimi
dana udani
phunzitsa mphunzitsi
konza mkonzi
Page 10 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
mwana mphepo mwanamphepo
Zitsanzo
Mneni Muonjezi Dzina
Page 11 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Kulumikiza mphatikiram’mbuyo ‘ku-’ ku tsinde la mneni
Zitsanzo
Mphatikiram’mbuyo Dzina
ku- kudya
ku- kumwa
ku- kuphunzira
ku- kusamba
MUTU 3 MLOWAM’MALO
Mlowam’malo ndi mawu omwe amaima kapena amalowa m’malo mwa dzina.
MITUNDU YA ALOWAM’MALO
Wa dzina lakelake
Alowam’malo olowa m’malo mwa dzina la munthu
a. Alowam’malo akalozamwini
Awa amalowa m’malo mwa dzina la munthu kapena anthu omwe akuyankhula.
Zitsanzo:
1. Ine ndavutika kwambiri.
2. Ife tipita mochedwa.
b. Alowam’malo akalozamnzako
Awa amalowa m’malo mwa dzina la munthu kapena anthu omwe akumvera zomwe wina
akuyankhula.
Zitsanzo:
1. Iwe, pita msanga.
2. Inu, thamangani munthu uja akuthawa.
3. Ndikuyankhula ndi inu.
Page 12 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
c. Alowam’malo akalozawina
Awa amalowa m’malo mwa dzina la munthu kapena anthu omwe tikuwatchula m’nkhani.
Munthuyu kapena anthuwo akhoza kukhala kuti ali kutali pang’ono kapena kwina kwake kotero
sakudzimvera zomwe zikunenedwa zokhudza iwowo.
Zitsanzo:
1. Iye wakhaula ndipo sadzabwerezanso.
2. Iwo apita lero.
Alowam’malo oloza
Alowam’malo oloza chinthu chomwe chili pafupi kapena choyandikira
Zitsanzo:
1. Uyu wamenya mwana.
2. Ichi ndi choipa.
3. Aka ndi kanga.
Alowam’malo aumwini
Zitsanzo:
1. Wake wabwera.
2. Chako ndi chako.
3. Zathu zalowa m’khola.
4. Wanga wabwera dzulo.
5. Ndationa tanu tikudya msipu.
6. Zanga zili paphiri.
Page 13 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Alowam’malo amgwirizano
Zitsanzo:
1. Amene afuna abwera.
2. Ndifuna zomwe zija.
3. Omwe agona asiyeni.
Alowam’malo odzichitira
Zitsanzo:
1. Wadzimenya yekha.
2. Mudzifunse nokha.
3. Khala pansi ungadzipweteke.
Alowam’malo otsimikiza
Zitsanzo:
1. Iye mwini wandifunsa za nkhaniyi.
2. Ine amene simungandimenye.
3. Ndine ndemwe ndaswa chikhochi.
Alowam’malo ofunsa
Zitsanzo:
1. Ukufuna ziti?
2. Wayani akubwera apo?
3. N’kuti wapitako?
Alowam’malo ochuluka
Zitsanzo:
1. Ndagula ziwiri zokha.
2. Anayi akubwera apo.
3. Mwalandira khumi.
NTCHITO ZA ALOWAM’MALO
Alowam’malo amatha kukhala eninkhani kapena pamtherankhani.
Eninkhani
a) Wa dzina lakelake
Zitsanzo
1. Ine ndimakonda mbatata yowotcha.
2. Iwo akumanga nyumba.
3. Iwe thawa njokayo.
b) Wa umwini
Zitsanzo
1. Zanga zabwera.
2. Chanu palibe.
3. Kwanu kuli bwino.
c) Wamgwirizano
Zitsanzo
1. Chimene chilibe ntchito tayani.
2. Amene afuna abwera.
3. Komwe wapita sikudziwika.
d) Woloza
Zitsanzo
1. Uyu pita nayeni.
2. Iyi yabwira ufa.
3. Ichi n’chimanga, icho n’chinangwa.
e) Wofunsa
Zitsanzo
1. Ndi ziti zagwera m’dzenje?
2. N’chotani watengacho?
Page 15 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
3. Muti umati ulowe?
f) Zochuluka
Zitsanzo
1. Ambiri apita kukasewera mpira.
2. Angapo achita ngozi.
3. Chochepa sichikwanira.
Apamtherankhani
a) Wa dzina lakelake
Zitsanzo
1. Joni amandinena ine.
2. Tawaona iwo akumenyana.
3. Amakunyoza iwe.
b) Waumwini
Zitsanzo
1. Mukanditengereko yanga.
2. Ndathana nacho chanu.
3. Ndizikakhala kwathu.
c) Wamgwirizano
Zitsanzo
1. Mwadya zomwezo.
2. Sindifuna zotere.
3. Ndamudziwa amene waba.
d) Woloza
Zitsanzo
1. Ndipatse ilo.
2. Osaponda apa.
3. Wamuona uja?
e) Wofunsa
Zitsanzo
Page 16 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
1. Ukufuna zotani?
2. Mukuyendera ziti?
3. Amakhala kuti?
f) Wochuluka
Zitsanzo
1. Ndadya zambiri.
2. Mundipatseko zochepa.
3. Tagwira angapo.
MUTU 4 MNENI
Mneni ndi mawu omwe amatidziwitsa zochitika.
MITUNDU YA ANENI
Mneni woyambukira
Ntchito ya mneniyu ndi kuwonetsa chinthu chomwe chagwira ntchito komanso chinthu chomwe ntchito
yachitikira pa icho.
Zitsanzo
1. Galu wapha bakha.
2. Amayi ataya makiyi.
Mneni wosayambukira
Uyu sakhala ndi pamtherankhani kotero ntchito yake sisonyeza kuti yachitikira yani.
Zitsanzo
1. Achimwene abwera lero.
2. Maliya wapita kale.
Page 17 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Magulu ena a aneni ali motere:
Mneni wophatikizika/wodalira
Uyu amadalira mawu omwe ayikidwa kutsogolo kwa mneniyo kuti ganizo limveke bwino.
Zitsanzo
1. Iyi ndi nkhono.
2. Chikondi simnzanga.
Mneni wothandizira
Uyu amathandizira mneni mnzake kuti ganizo limveke bwino.
Zitsanzo
1. Mphatso ali kugulitsa njinga.
2. Kodi muli kuyankhula ndi yani?
Zitsanzo
1. Tawonjeza thobwa mkapumo.
2. Wamaliza nsima yonse yekha.
Page 18 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Okhala ndi tsinde la maphatikizo asanu
Zitsanzo
1. Tambalikiza kuti anthu apatsidwawo amve uthengawu.
2. Bulubudira ndi bulangete chifukwa wazizidwa kwambiri.
NTHAWI ZA ANENI
Nthawi ya mneni ndi kakhalidwe ka mneni komwe kamasonyeza nthawi yomwe ntchito inachitika, ichitike
kapena idzachitike.
Zitsanzo
1. Tidakhala tikuyembekezera galimoto usiku wonse.
2. Anakhala akundinamiza kwa nthawi yayitali.
Page 19 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
ii) Nthawi yatsopano
Kusonyeza ntchito zochitika kawirikawiri makamaka chifukwa choti ndi ntchito kapena khalidwe la
wochitayo.
Zitsanzo
1. Mulungu amakukondani.
2. Iwo amalima mpunga.
MSINTHO WA ANENI
Uku ndi kusintha kwa ntchito ya mneni poika aphatikiri ku tsinde la mneni kuti mneniyo apereke
tanthauzo lina kapena losinthika.
Page 21 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Chipupa chamangika bwino.
c. Msintho wonyazitsa
Zitsanzo
1. Katswiri wa nkhonya uja wamenywa kwambiri.
2. Munthu uja wapezwa lero.
3. Galu wawo waphewa.
d. Msintho wom’chitira
Umasintha poyika aphatikiram’tsogolo awa: -ira, -era.
Zitsanzo
1. Achimwene andigulira malaya.
2. Alinafe amubera zovala.
e. Msintho wochititsa
Umasonyeza chomwe chayambitsa kuti ntchito ichitike ndipo umasintha poyika
aphatikiram’tsogolo awa: -etsa, -itsa.
Zitsanzo
1. Munthu wathawitsa mbalame.
2. Mkazi wachiwerewere waphetsa mwamuna.
f. Msintho wochititsitsa
Umasonyeza kuti ntchito yachitika mopitiriza muyeso kapena kuti yachitika kwambiri ndipo aneni
amasintha poyika aphatikiram’tsogolo awa: -etsetsa, -itsitsa.
Zitsanzo
1. Penyetsetsa kuti uwone zenizeni.
2. Funsoli lavutitsitsa sindilembanso.
g. Msintho wochitirana
Page 22 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
h. Msintho wotsutsana
Umasonyeza kutsutsana kwa ntchito yomwe yachitika ndipo aneni ake amasintha pochotsa lembo
la ‘a’ lotsiriza kwa mneni ndi kuika m’phatikiram’tsogolo –ula
Zitsanzo
Mneni Msintho wotsutsana nawo
tseka tsekula
yala yalula
mata matula
i. Msintho wobwerezabwereza
Umasonyeza kubwerezabwereza kwa ntchito ndipo umasintha pongobwereza ntchito/tsinde la
mneni.
Zitsanzo
1. Usamadutsadutsa msewu njinga zingakugunde.
2. Mkazi wokwatiwa sapitapita kwa makolo ake.
MUTU 5 MFOTOKOZI
Mfotokozi ndi mawu omwe amatidziwitsa (amafotokoza) zambiri za dzina kapena mlowam’malo.
MITUNDU YA AFOTOKOZI
Page 23 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Mfotokozi wa mkhalidwe
Mfotokoziyu amanena za khalidwe la dzina kapena mlowam’malo. Mfotokoziyu amapangidwa
kuchokera ku mayina, aneni, aonjezi ndi mvekero.
Zitsanzo
a. Iwo akumana ndi anthu achifwamba.
b. Atatu achiwewe aluma mbuzi.
c. Munthu wakuba sakondedwa.
d. Ena abwino sakhalitsa padziko.
3. Mfotokozi wa umwini
Uyu ndi mfotokozi yemwe amasonyeza umwini ndipo amapangidwa pophatikiza
aphatikiram’mbuyo ku masinde a umwini.
Zitsanzo
a. Uja ndi mwana wanga.
b. Kuimba kwake kwandisangalatsa.
c. Galu wako ndi waukali.
d. Dzina lathu ndi lamtendere.
4. Mfotokozi woloza
Uyu ndi mfotokozi yemwe timagwiritsa ntchito poloza dzina. Afotokozi ena oloza amapangidwa
pophatikiza aphatikiram’mbuyo ku masinde oloza n’kupanga alozi.
Zitsanzo
a. Khasu ili ndi la amayi.
b. Chala ichi chatupa.
c. Pamudzi pano pali mbava.
d. Ndamuona mwana uja.
Mfotokozi wochuluka
5.
Mfotokozi uyu amasonyeza kuchuluka kwa zinthu. Mfotokozi uyu ali ndi mitundu yakeyake itatu
iyi:
i) Mfotokozi wowerenga
Mfotokoziyu amawerenga mayina kapena alowam’malo ndipo amachokera ku masinde a
mawerengo ‘-modzi’, ‘-wiri’, ‘-tatu’, ‘-nayi’ ndi ‘-sanu’.
Zitsanzo
a. Ndadya mbamu ziwiri.
b. Iye watsala madzi amodzi.
c. Ana asanu abwera kale.
d. Ndikufuna zinthu zitatu.
Page 24 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
ii) Mfotokozi wogawa
Mfotokoziyu amakamba za mayina kapena alowam’malo omwe ali pagulu
pawokhapawokha. Mfotokoziyu amapangidwa kuchokera kutsinde ‘-li-nse’ ndipo
amalembedwa ngati mawu amodzi.
Zitsanzo
a. Abwera wina aliyense.
b. Nkhuni iliyonse pamtolopo ndi yaiwisi.
c. Mundigawire chimanga chilichonse.
6. Mfotokozi wamgwirizano
Mfotokoziyu amapangidwa kuchokera ku masinde a mgwirizano ‘-mene’ ndi ‘-mwe’.
Zitsanzo
a. Munthu amene waba sindinamuone.
b. Ili ndi buku lomwe ndimafuna.
c. Ophunzira omwe akhoza mayeso akusangalala.
d. Undiuze chinthu chimene chikukuvuta.
7. Mfotokozi wofunsa
Mfotokoziyu ndi mawu wofunsira omwe amafuna kudziwa zambiri za dzina kapena mlowam’malo.
Mfotokozi amapangidwa kuchokera ku masinde ofunsira awa: ‘-tani’, ‘-ti’, ‘-nji’, ‘-yani’, ndi ‘-ngati’.
Zitsanzo
a. Mwagula nkhuku zingati?
b. Ndi galu wayani waluma mwana?
c. Awa ndi makhalidwe anji?
d. Kodi iye wagwetsa mtengo uti?
e. Ukufuna zinthu zotani?
Page 25 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 6 MUONJEZI
Muonjezi ndi mawu omwe amanena zambiri za mfotokozi, mneni kapena muonjezi mnzake.
MITUNDU YA AONJEZI
1. Muonjezi wa mchitidwe
Muonjeziyu amafotokoza za momwe ntchito yachitikira.
Zitsanzo
a. Ife tafika bwino.
b. Anatilandira mwansangala dzulo.
c. Yohane amaganiza mwachibwana.
d. Nyembezi amayankhula monyada.
e. Nkhono imayenda pang’onopang’ono.
2. Muonjezi wa nthawi
Muonjeziyu amafotokoza nthawi yomwe ntchito yachitikira.
Zitsanzo
a. Anandigogodera m’bandakucha.
b. Mubwere kwathu masana.
c. Makedzana kunali ana opanda mwano.
d. Sindinamuone chichere.
e. Makono kwachuluka achifwamba.
3. Muonjezi wa malo
Muonjeziyu amasonyeza komwe ntchito inachitikira.
Zitsanzo
a. Ndamuona, ali kuno.
b. Buluzi aligone pamwala.
c. Galimoto yagwera m’mtsinje.
d. Musalowe muno.
e. Bwera pano, mnzanga.
Muonjezi wa muyeso
4.
Muonjeziyu amapima kuchepa kapena kukula kwa momwe ntchito yachitikira.
Zitsanzo
a. Iye wavulala kwambiri pangoziyo.
b. Wamwa pang’ono.
Page 26 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Muonjezi wa muyeso ali ndi mitundu yakeyake yotsatirayi:
i) Wa muyeso wosonyeza kuwerenga
Muonjeziyu amawerenga kuti ntchito yachitika kangati.
Zitsanzo
a. Wabweranso kachitatu.
b. Ndagogoda kawiri koma sanandiyankhe.
c. Iye amapita kwawo kamodzikamodzi.
d. Anagwa kasanu ndi njinga.
Page 27 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 7 MLUMIKIZI
Mlumikizi ndi mawu omwe amagwira ntchito yomangiriza mawu, akapandamneni kapena ziganizo.
MITUNDU YA ALUMIKIZI
1. Mlumikizi woluzanitsa (wophatikiza)
Mlumikiziyu amaika pamodzi mawu, akapandamneni kapena ziganizo.
Zitsanzo
a. Andigulira malaya ndi nsapato.
b. Jeketeli ndi lopepuka komanso lofunda.
c. Ine ndadya ndipo ndakhuta.
2. Mlumikizi wopatula
Mlumikiziyu amalekanitsa kapena kutayanitsa mawu, akapandamneni kapena ziganizo potsutsa
ganizo la mawu olumikizidwawo.
Zitsanzo
a. Ndikufuna mpunga osati nsima.
b. Anayesetsa kulimbikira koma walephera.
c. Mundipatse ndalama zanga osati chakudya.
3. Mlumikizi wamgwirizano
Mlumikiziyu amayanjanitsa mawu, akapandamneni kapena ziganizo pokamba za chifukwa
chochitira kanthu.
Zitsanzo
a. Iye wabwera chifukwa akudwala.
b. Poti mwatero, ndipita.
c. Sindifusanso popeza mwandilangiza.
4. Mlumikizi wazotsatira
Mlumikiziyu amaonetsa zolinga kapena zotsatira za ntchito.
Zitsanzo
a. Sankawerenga choncho walephera mayeso.
b. Amamuseka wodwala misala kotero wamumenya.
c. Pempha kuti akupatse.
Page 28 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
NTCHITO ZA ALUMIKIZI
Alumikizi amagwira ntchito zosiyanasiyana m’ziganizo. Ntchitozo n’zofanana ndi mitundu ya alumikiziwo.
Ntchitozo zili motere:
1. Kuphatikiza
Zitsanzo
a. Abambo ndi amayi amalima kwambiri.
b. Anaphika nsima ndipo adya.
c. Mwana wake ndi wanzeru komanso waulemu.
2. Kutayanitsa/kulekanitsa
Zitsanzo
a. Ugule nsomba osati nyama.
b. Iye ndi wamwano koma mnzake ndi waulemu.
c. Ndikufuna ndalama osati zovala.
3. Kugwirizanitsa
Zitsanzo
a. Mupitebe poti atero.
b. Iye sabwera chifukwa akudwala.
c. Sindifusanso popeza mwandiseka.
Kusonyeza zotsatira/zolinga
4.
Zitsanzo
a. Pempha kuti akugawireko.
b. Anatopa kotero waweruka.
c. Sankalimbikira choncho walephera.
Page 29 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 8 MPEREKEZI
Mperekezi ndi mawu omwe amatsata dzina kapena mlowam’malo pofuna kuonetsa mgwirizano pakati pa
dzinalo kapena mlowam’maloyo ndi mneni m’chiganizo.
MITUNDU YA APEREKEZI
Aperekezi amaikidwa mu mitundu yosiyanasiyana. Mitunduyo ili motere:
1. Mperekezi wosonyeza malo
Mperekeziyu amagwira ntchito yosonyeza malo kapena mbali.
Zitsanzo
a. Ndipita ku Lilongwe mawa.
b. Pa Linthipe panachitika zoopsa.
c. Sungayende wekha mu Blantyre.
Zitsanzo
a. Amumenya ndi ndodo.
b. Usanditengere ku mtoso ngati njoka.
c. Iye adzabwera pa ngolo.
Page 30 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
5. Mperekezi wosonyeza mgwirizano
Mperekeziyu amakhala ngati wa umwini koma sic honcho chifukwa amagwira ntchito
yongosonyeza mgwirizano.
Zitsanzo
a. Iye wabisala kuseli kwa nyumba.
b. Dziko la Malawi ndi lamtendere.
c. Iye ali ndi mankhwala amphamvu.
NTCHITO ZA APEREKEZI
Aperekezi amagwira ntchito zosiyanasiyana m’ziganizo molingana ndi mitundu yawo. Ntchitozo zili
motere:
1. Kusonyeza mbali kapena malo
Zitsanzo
a. Iye amakhala ku Salima.
b. Ukatsikire pa Malosa.
c. Tikapezana mu Limbe.
2. Kusonyeza umwini
Zitsanzo
a. Mbuzi ya Lazalo yapezeka.
b. Wapulumikira m’kamwa mwa mbuzi.
c. Chipewa cha Naphiri n’cholimba.
3. Kusonyeza nthawi
Zitsanzo
a. Ndidzapita kwathu pa 11 Juni.
b. Mvula imayamba kugwa mu Novembala.
c. Sindinakumane naye kwa masiku asanu tsopano.
Kusonyeza chipangizo
4.
Zitsanzo
a. Amubaya ndi mkondo.
b. Musanditengere ku mtoso.
c. Iye adzabwera pa galimoto.
Page 31 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
5. Kusonyeza mgwirizano
Zitsanzo
a. Musamalime m’mbali mwa mtsinje.
b. Phiri la Mulanje ndi lokongola.
c. Mtsogoleriyu ali ndi chikoka.
MUTU 9 MFUWU
Mfuwu ndi mawu omwe amagwiritsidwa ntchito mofuwula pofuna kusonyeza momwe zochitika
zamukhudzira yemwe zamuchitikira.
Mawuwo amasonyeza kudabwa, kukondwa, kunyansidwa, kuwawidwa, kumva chisoni, kudandaula,
kukopa chidwi ndi kulimbikitsa.
Mawuwa amathera ndi chizindikiro cha m’kalembedwe cha mfuwuliro.
Zitsanzo
a. Mayo!
b. Kalanga ine!
c. Hehede!
MITUNDU YA MFUWU
Mifuwu imaikidwa mu mitundu yosinasiyana.
Zitsanzo
a. Ha! Mwanayu ndi wamwano chotere?
b. Kani! Sindinadziwe kuti munakhumudwa.
c. Aa! Zakhala chonchi?
Page 32 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Mfuwu wosonyeza kuvomereza
Zitsanzo
a. Ame! Mulungu ndi wabwino.
b. Odini! Fikani, takulandirani.
c. Ataibaya nyamayo, ndinamva kuti shomo!
NTCHITO ZA MIFUWU
Mifuwu imagwira ntchito zosiyanasiyana ikakhala payokha kapena m’ziganizo. Kawirikawiri ntchito za
mifuwu zimagwirizana ndi mitundu yake. Ntchitozo zili motere:
1. Kudabwa
Zitsanzo
a. Ha! Moti uyu ndi mwana wanu.
Page 33 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
b. Kani! Sindimadziwa kuti mungandithandize.
c. Aa! Sindimayembekeza kuona zotere.
2. Kuvomereza
Zitsanzo
a. Ame! Mulungu akudalitseni.
b. Odini! Fikani.
c. Ndangomva kuti shomo!
4. Kukondwa
Zitsanzo
a. Gule wakoma; woyee!
b. Hehede! Ndapambana mayeso.
c. Takondwa! Mwana wathu wakwatiwa.
Kulimbikitsa
5.
Zitsanzo
a. Malawi, chinya!
b. Ponya chibakera, gwetsa!
c. Gwira! Tidyere nyama.
Kukopa chidwi
6.
Zitsanzo
a. Mtendere! Tikhale pansi.
b. Aleluya! Mulungu ndi wabwino.
c. Bungwe lathu, motoo!
Page 34 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 10 MVEKERO
Mvekero ndi maliwu kapena mawu omwe amapereka ganizo.
Mimvekero imatha kuima payokha (mosathandizidwa ndi mawu ena) n’kupereka ganizo lamveka bwino.
MAGULU A MIMVEKERO
Mimvekero imaikidwa m’magulu molingana ndi chiwerengero cha maphatikizo mu tsinde la mvekero.
1. Mimvekero ya tsinde la phatikizo limodzi
Zitsanzo
psuu guu ndi nji phaa phi thi
Zitsanzo
tsitu ngunda fwasu gwedze psiti yazi phava
khutcha thapsa vwapa waka tswere pholi thathya
Zitsanzo
likhwithi dangali dululu gubidi pwepwete ngumbali kakasi
Zitsanzo
Page 35 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
thakwalala pholokoto polokotso thasalala gulupati yangalala
MITUNDU YA MIMVEKERO
1. Mimvekero ya maonekedwe
Mimvekero ya m’mtunduwu imakamba za mtundu (kaonekedwe) wa zinthu.
Zitsanzo
a. Maso ako ali psu.
b. Kunja kwangoti ngwe.
c. Zovala zayera kuti mbe.
d. M’mera uli biriwiri m’munda.
e. Chidakwa chili bi ngati mtsiro.
2. Mimvekero ya mamvekedwe
Mimvekero ya m’mtunduwu imakamba za mamvekedwe a zinthu pathupi, m’makutu, m’kamwa
ndi m’mphuno.
Zitsanzo
a. Thupi lako lili juu. Kodi ukudwala?
b. Buluzi wagwa kuti phofo.
c. Ukamva kuti nginde, ndiye kuti afika.
d. Manyuchi ali tseketseke.
e. Mwagula sopo yabwino, ili guu.
Page 36 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
3. Mimvekero ya mkhalidwe
Mimvekero ya m’mtunduwu imakamba za kakhalidwe ka chinthu.
Zitsanzo
a. Mtengowu uli nji.
b. Vumbwe ali bisale patchire.
c. Mwangoti du; kodi mwatani?
d. Ndisenza ndekha mtolowu; uli pepu.
e. Ali sukwasukwa chifukwa cha mantha.
4. Mimvekero ya mchitidwe
Mimvekero ya m’mtunduwu imakamba za kachitidwe ka ntchito.
Zitsanzo
a. Nyani ali chinyachinya m’munda.
b. Wangoti m’nyumba gubidi, atandiona.
c. Chidakwa chili dzandidzandi.
d. Msampha wangoti fwamphu.
e. Ali yakaliyakali kuthamangira kumsika.
Zitsanzo
1. a. Wanu wabwera dzulo. (mlowam’malo)
b. Mwana wanu wabwera dzulo. (mfotokozi)
Page 37 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. a. Ndagula zitatu. (mlowam’malo)
b. Ndagula mbuzi zitatu. (mfotokozi)
Kufananirako kwa mlowam’malo ndi mfotokozi ndi koti mitundu yambiri ya mlowam’malo ndi
yomweyonso ya mfotokozi.
Mitunduyo ndi monga yaumwini, yochuluka, yofunsa, yoloza ndi yamgwirizano.
Zitsanzo
1. a. Lathu ndi lokongola. (mlowam’malo waumwini)
b. Dziko lathu ndi lokongola. (mfotokozi waumwini)
Chenjezo
Alowam’malo a dzina lakelake akatsatana ndi mayina amaoneka ngati afotokozi chifukwa amakhala
pamalo pomwe afotokozi amakhala. Alowam’malo amenewa amakhalabe alowam’malo osati afotokozi.
Kumbutso
Ena amaganiza kuti dzina likangochotsedwa ndiye kuti nthawi yomweyo mfotokozi (mawu wokamba
zambiri za dzinalo) amasanduka dzina kapena mlowam’malo monga zimakhalira mu chingerezi. Izi sizili
choncho; mfotokoziyo amakhalabe mfotokozi chifukwa Chichewa chili ndi khalidwe lotaya mchitantchito
kapena mchitidwantchito.
Zitsanzo zabwino za afotokozi otere ndi omwe amapangidwa kuchokera ku mayina, aneni, aonjezi ndi
masinde enieni a mfotokozi.
Chitsanzo
- Munthu wakufa sadziwika.
Page 38 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
M’chiganizochi mfotokozi ndi mawu woti ‘wakufa’ chifukwa akukamba zambiri za dzina ‘munthu’.
Tikachotsa dzina loti ‘munthu’, titsala ndi mfotokozi ‘wakufa’. Mawu woti ‘wakufa’ akhalabe mfotokozi
chifukwa akukamba zambiri za dzina lomwe latayidwa.
Mphatikiram’mbuyo ‘wa’ mu ‘wakufa’ akutsimikiza kuti mawuwa akukamba za mawu ena omwe ali nawo
pamgwirizano ngakhale tawachotsa.
Zitsanzo zina
a. Amoyo salekana.
b. Wabwino ali kuti?
c. Wokongola sanyada.
d. Wachitatu n’kapasule.
e. Chamuluma ndi chakuda.
Kumbutso
Afotokozi angapo okamba za dzina limodzi amatha kutsatana mwadongosolo m’chiganizo chimodzi.
Zitsanzo
a. Mbuzi zakuda zonse zisanu zafa.
b. Mwana wanu wamtali wofatsa uja ndi wamwano.
c. Sindinaonepo galu wamkazi wachizungu wokalamba chonchi.
MUTU 12 CHIGANIZO
Chiganizo ndi mawu kapena gulu la mawu lokhala ndi mneni ndipo limapereka ganizo lathunthu.
Zitsanzo
1. Ndakhuta.
2. Ine ndadya nsima.
3. Mtengo uja wagwa.
4. Katangale ndi woipa.
Mawu ofunikira kwambiri kuti chiganizo chimveke bwino komanso kupereka tanthauzo ndi awa:
mchitantchito, mneni ndi mchitantchito.
Komabe si ziganizo zonse zomwe zimakhala ndi mchitantchito.
Page 39 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MAGAWO A CHIGANIZO
Chiganizo chilichonse chimakhala ndi magawo aakulu awiri.
Magawo awiriwo ndi awa: gawo losonyeza yemwe wachita ntchito ndi gawo losonyeza ntchito yomwe
yachitika.
Gawo losonyeza yemwe wachita ntchito limatchedwa ‘mchitantchito’ (mwininkhani) ndipo gawo lomwe
limasonyeza ntchito yachitika limatchedwa ‘mnenankhani’.
Zitsanzo
1. Uyu si mzanga.
2. Mwana wadya phala.
3. Munthu waulesi satukula dziko.
4. Amayi ndi Abambo apita kumunda.
5. Mvula yamasiku ano ndi yanjomba.
Mchitantchito (mwininkhani) Mnenankhani
1. Uyu si mzanga
2. Mwana wadya phala
3. Munthu waulesi satukula dziko
4. Amayi ndi Abambo apita kumunda
5. Mvula yamasiku ano ndi yanjomba
MITUNDU YA ZIGANIZO
Ziganizo zimaikidwa mu mitundu yaikulu yotsatirayi.
Page 40 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Chiganizo cha ziganizo zingapo
Chiganizo cha ziganizo zingapo chimakhala ndi ziganizo zina m’kati mwake. Ziganizo zingapozo
zimaluzanitsidwa ndi mlumikizi.
Mnenankhani wa chiganizochi amakhala ndi aneni angapo.
Chitsanzo
- Ine ndadya nsima ndipo ndakhuta. (Mu chiganizochi muli ziganizo ziwiri: Ine ndadya nsima ndi
(Ine) ndakhuta. Ziganizo ziwirizi zaluzanitsidwa ndi mlumikizi ‘ndipo’.)
Zitsanzo zina
a. Agogo ake sasuta fodya koma amamwa mowa.
b. Ife talemba mayeso ndipo tapambana.
c. Alendo athu anabwera koma akhumudwa choncho apita kwawo.
Dziwani izi: ziganizo zomwe zimapanga chiganizo cha ziganizo zingapo zimakhala ziganizo zopanda
nthambi.
TIDZIWE: Tisasokoneze “chiganizo cha ziganizo zingapo” ndi “chiganizo cha nthambi”. Ziganizo zomwe
zimapanga chiganizo cha ziganizo zingapo zimatha kuima pazokha n’kupereka ganizo pomwe chiganizo
cha nthambi chimakhala ndi chiganizo chimodzi chokha chopereka ganizo ndipo kagulu ken aka mawu
kokhala ndi mneni kamadalira chiganizo chimodzicho kuti kapereke ganizo.
Page 41 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
4. Chiganizo cha ziganizo zanthambi
Chiganizochi chimakhala ndi nthambi yoima payokha imodzi ndi nthambi zosaima pazokha zingapo.
Chitsanzo
- Tili m’tulo, mbava zinalowa m’nyumba ngakhale panja panali alonda.
Mu chiganizo chili pamwambachi, nthambi yoima payokha ndi ‘mbava zinalowa m’nyumba’.
Tikaonetsetsa bwino mu chiganizochi muli nthambi zosaima pazokha ziwiri izi: ‘tili m’tulo’ ndi ‘ngakhale
panja panali alonda’.
Zitsanzo zina
a. Gogo Chirwa anadodoma zedi atamva Mzungu akuyankhula Chitonga popeza adali asadamvepo
zotere.
b. Ngakhale anatipeza tisanayambe kudya, iwo sanadye nafe chifukwa sadya kwa eni.
c. Mvula ikagwa bwino, tikolola chimanga chambiri poti tachita zonse zofunikira zomwe mlangizi
anatiuza.
Chiganizo (nthambi yoima payokha) Nthambi zingapo mu chiganizo
1. Gogo Chirwa anadodoma zedi a. atamva Mzungu akuyankhula Chitonga
b. popeza adali asadamvepo zotere
2. Iwo sanadye nafe a. ngakhale anatipeza tisanayambe kudya
b. chifukwa sadya kwa eni
3. Tikolola chimanga chambiri a. mvula ikagwa bwino
b. poti tachita zonse zofunikira
c. zomwe mlangizi anatiuza
Mudzaphunzira zambiri za nthambi za chiganizo mu gawo la ‘Nthambi za chiganizo’.
Zitsanzo
a. Iye ndi Tionge apita kwawo dzulo.
b. Nyama zakutchire zimakopa alendo.
c. Makolo anga amandipatsa malangizo abwino nthawi zonse.
Mchitantchito Mchitidwantchito
a. Iye ndi Tionge apita kwawo dzulo
b. Nyama zakutchire zimakopa alendo
c. Makolo anga amandipatsa malangizo abwino nthawi zonse
Page 42 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Kusanthula mchitantchito, mchitidwantchito, mneni ndi ziwonjezero zawo
i) Chiwonjezero cha mchitantchito ndi mawu kapena kagulu ka mawu kamene kamafotokoza
zambiri za mwininkhani
ii) Chiwonjezero cha mchitidwantchito ndi mawu kapena kagulu ka mawu kamene kamakamba
zambiri za mchitidwantchito
iii) Chiwonjezero cha mneni ndi mawu kapena kagulu ka mawu kamene kamakamba zambiri za
mneni. Kawirikawiri chiwonjezero cha mneni chimakhala muonjezi kapena kapandamneni wa
muonjezi.
Zitsanzo
a. Ana omva mwambo sanyoza makolo awo nthawi zonse.
b. Ife tonse tagula zinthu zabwino motchipa kumsika.
c. Mtsikana wokongola uja anaba mafuta onunkhira dzulo kusitolo.
Mchitantchito Chionjezero cha Mneni Chionjezero Mchitidwantchito Chionjezero cha
mchitantchito cha mneni mchitidwantchito
Ana omva mwambo sanyoza nthawi zonse makolo awo
Ife tonse tagula motchipa zinthu zabwino
kumsika
Mtsikana wokongola uja anaba kusitolo dzulo mafuta onunkhira
NTHAMBI YA CHIGANIZO
Nthambi ya chiganizo ndi gulu la mawu m’chiganizo lomwe limakhala ndi mchitantchito (mwininkhani) ndi
mnenankhani.
M’chitsanzochi, mchitantchito wa chiganizo ndi ‘Nkhanga’ ndipo mnenankhani yemwe akugwirizana ndi
mchitantchitoyo ndi ‘zinapangana’. Mogwirizana ndi tanthauzo la nthambi yoima payokha ndiye kuti
m’chitsanzochi, nthambi yoima payokha ndi ‘Nkhanga zinapangana’ chifukwa ikupereka ganizo lamveka
bwino poyerekeza ndi nthambi ina yomwe yatsala: ‘kunja kusanapse’.
Mu chiganizo ‘Nkhanga zidapanga kunja kusanapse’, nthambi yomwe sikuima payokha ndi “kunja
kusanapse”. Nthambiyi ndi nthambi yosaima payokha ndipo ikudalira nthambi yoima payokha (Nkhanga
zinapanga) kuti ipereke ganizo.
Zitsanzo zina
1. Ndi zoona zoti iye ndi m’nzanga.
2. Galimoto yomwe agula yachita ngozi.
3. Ngakhale ulire, sindikupatsa ndalamayo.
4. Mvula ikugwa mwanjomba chifukwa nyengo ikusintha.
5. M’mene unkabwera, udali mwana wabwino.
Nthambi yoima payokha Nthambi yosaima payokha
1. Ndi zoona zoti iye ndi m’nzanga
2. Galimoto yachita ngozi yomwe agula
ngakhale ulire
3. Sindikupatsa ndalamayo
4. Mvula ikugwa mwanjomba chifukwa nyengo ikusintha
5. Udali mwana wabwino m’mene unkabwera
NTHAMBI YA DZINA
Nthambi ya dzina ndi nthambi yosaima payokha yomwe imagwira ntchito ngati dzina. Nthambiyi ndi
yankho la funso ‘chiyani’ kapena ‘kuti chiyani’ kapenanso ‘-yani’ ndi ‘-ti’.
Zitsanzo
a. Ndi zabodza zoti John wabwera.
b. Sadaulule zomwe anagwirizana.
c. Unene chomwe chayambitsa mkanganowu.
d. Zoti amadyera nyama, si zachilendo.
e. Ndimadziwa kuti atolankhani ena amalemba zopsetsa mtima.
f. Ife tamva zimene mwapangana.
Zitsanzo
a. Izi ndi zomwe umafuna.
b. Zinthu wagulazo si zimene ndinakutuma.
c. Kamuzu anali munthu yemwe ankakonda ulimi.
NTHAMBI YA MFOTOKOZI
Nthambi ya mfotokozi ndi nthambi yosaima payokha yomwe imagwira ntchito ngati mfotokozi. Nthambiyi
imakamba zambiri za dzina kapena mlowam’malo.
Nthambiyi ndi yankho la funso ‘-ti?’ kapena ‘-tani?’. Nthawi zambiri nthambiyi imayamba ndi mawu a
mgwirizano (ochokera ku masinde ‘-mene’ kapena ‘-mwe’).
Zitsanzo
a. Zitatu zomwe zaphedwa ndi zanga.
b. Ntchito imene munandilonjeza si imeneyi.
c. Kumudzi komwe ndinabadwira ndi kuno.
d. Msungwana akubwera apoyo sindimudziwa.
e. Munthu wofuna kupambana mayeso ayenera kulimbikira.
Page 45 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
NTHAMBI YA MUONJEZI
Nthambi ya muonjezi ndi nthambi yosaima payokha imene imagwira ntchito ngati muonjezi.
Nthambiyi ili ndi mitundu yakeyake yambiri molingana ndi ntchito zomwe nthambizo zimagwira.
Zitsanzo
Amaimba monga m’mene amaimbira amake.
Iye akuyenda ngati watopa.
Mphaka amadya monga safuna.
Zitsanzo
Komwe wachedwa msulu, kuli nyerere.
Ndabisa ndalamazo pamene wina sangazione.
Mubzale mbewuzo momwe muli chinyontho.
Zitsanzo
Iye anadabwa madzi atamufika m’khosi.
Mmene munkabwera, munali anthu abwino.
Nthawi yomwe mwamva m’mimba, imwani mankhwala.
Zitsanzo
Papsa tonola poti sudziwa mtima wa moto.
Wamenyedwa chifukwa anamuyamba wodwala misala.
Popeza wandinyoza, sindidya nsima yanu.
Page 46 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
e. Nthambi ya muonjezi wa cholinga
Nthambiyi imatiuza ‘cholinga’ chogwirira ntchito. Nthawi zambiri nthambiyi imayankha funso loti
‘chifukwa chiyani’ (ngakhale simanena za ‘chifukwa’ koma za cholinga). Kawirikawiri nthambiyi
imayamba ndi mawu woti ‘kuti’.
Zitsanzo
Yesu anafa kuti tipulumuke.
Bwerani mudzaone zomwe ndakugulirani.
Akuphunzira n’cholinga choti achotse umbuli.
Zitsanzo
Sindipitabe ngakhale mundinyengerere.
Angakhale mukane chakudyachi, mwalepherabe mayeso.
Chinkana mulire, sundikuthandizanibe.
Zitsanzo
Sindipita kumphwandoko pokhapokha andiitane.
Ngati abwera, ndipita nawo ku Lilongwe.
Mutagwira ntchitoyo mwaluso, ndingakulipireni moyenera.
Pamene tigwiritsa ntchito mphatikiri ‘-ta-’ pofuna kuonetsa upokhapokha, tiyenera kukumbukira kuti
mneni wa nthambi yoima payokha azikhala ndi mphatikiri ‘-nga-’.
Zitsanzo
Atabwera, ndingasangalale.
Mungayankhe mosavuta atakufunsani.
Zitsanzo
Joni waledzera kwabasi moti akungodzigwetsa.
Amalawirira kwambiri kotero simungamupeze.
Mwana wanu anandipsetsa mtima kwambiri mpaka ndamukalipira.
Page 47 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
KUPHWANYA CHIGANIZO POUNIKA MAWU PAWOKHAPAWOKHA
Kuphwanya chiganizo pounika mawu pawokhapawokha ndi ntchito yozukuta mawu opanga chiganizo
pawokhapawokha.
Mawu aliwonse amaunikidwa pawokha poona chilichonse chokhudza mawuwo.
Dzina : mtundu, chachimuna kapena chachikazi, ntchito, chimodzi kapena zambiri ndi gulu
Mlowam’malo : mtundu, chimodzi kapena zambiri ndi ntchito
Mfotokozi : mtundu
Zitsanzo
1. Iye wagula chipewa choyera mbee.
a. Iye : mlowam’malo, wa dzina lakelake, wakaloza wina, mchitantchito, chimodzi
b. wagula : mneni, woyambukira, kanenedwe kofotokoza, nthawi yatsopano yathayi,
kachitidwe ka wochita
c. chipewa : dzina, lopanda mwinimwini, si chachimuna kapena chachikazi, mchitidwantchito,
chimodzi, Chi-, Zi-
d. choyera : mfotokozi, wamaonekedwe
e. mbee : mvekero, waphatikizo limodzi, wamaonekedwe
Page 48 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 13 KAPANDAMNENI
Kapandamneni ndi mawu kapena gulu la mawu lothandiza kupanga chiganizo ndipo limagwira ntchito
ngati mtundu umodzi wa mawu koma silipereka ganizo chifukwa pafupifupi nthawi zonse silikhala ndi
mneni.
Chitsanzo
- Mnyamata wonyozeka uja anapeza ntchito yabwino kwambiri chaka chatha ku Lilongwe.
Mu chiganizo chili pamwambapa, mneni ‘anapeza’ akachotsedwa, mupeza kuti muli magulu a mawu
monga awa:
1. mnyamata wonyozeka uja
2. wonyozeka uja
3. ntchito yabwino kwambiri
4. yabwino kwambiri
5. chaka chatha
6. ku Lilongwe
Magulu a mawuwo ndi akapandamneni chifukwa akugwira ntchito ngati mtundu umodzi wa mawu koma
sakupereka ganizo pa iwo wokha.
MITUNDU YA AKAPANDAMNENI
Mitundu ya akapandamneni imachokera pa ntchito zomwe gulu la mawu limagwira.
Page 49 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Ntchito ya kapandamneni wa dzina Chitsanzo cha kapandamneni
1. Kukhala mchitantchito Bambo ndi mayi akuphika.
2. Kukhala mchitidwantchito Galu wagwira nkhuku yachitopa ija.
3. Kukhala olandira chinthu Ndamugulira mwana wanu malaya.
4. Kukhala mwini chinthu Ichi ndi chuma cha Mkazi wamasiye.
5. Kukhala mchitidwantchito wa mperekezi Wandimenya ndi ndodo yachitsulo.
6. Kukhala mawu apadera Nadzimbiri, mwana waulemu, wabwera.
7. Kukhala mtsirizitsi Malawi ndi dziko lamtendere.
8. Kuitanira Mwana wa a Banda, bwera kuno.
9. Kusonyeza malo
Apita kwa Mfumu yaikulu Gomani.
2. Kapandamneni wa mfotokozi
Ili ndi gulu la mawu lomwe limagwira ntchito ngati mfotokozi popeza limakamba zambiri za dzina kapena
mlowam’malo.
Zitsanzo
a. Mpeni wanga wotsopano uja wasowa.
b. Wandiphikira nsima yolumpha moto.
c. Mwana wanu wamng’ono akucheza ndi mzungu.
d. Zitatu zamawangamawanga zija zapezeka.
e. Munthu wosasunga mwambo salemekezedwa.
3. Kapandamneni wa muonjezi
Ili ndi gulu la mawu lomwe limagwira ntchito ngati mfotokozi.
Zitsanzo
a. Iwo amayankhula mopsetsa mtima.
b. Madalitso wabisala kuseli kwa nyumba.
c. Ife tabwera dzulo usiku kwambiri.
4. Kapandamneni wa mfuwu
Kapandamneni wa dzina lochikera ku mneni amagwira ntchito zina zomwe mayina kapena alowam’malo
amagwira.
6. Kapandamneni wa mperekezi
Ili ndi gulu la mawu lomwe limagwira ntchito ngati mperekezi.
Zitsanzo
a. Ndakumana ndi munthu wodabwitsa kwambiri.
b. Iye wadya phala la mwana.
c. Ku Blantyre kuli nyumba zamakono.
d. Mayi uja adakwatiwa ndi mzungu.
1. Mpumiro
Ichi ndi chizindikiro chomwe chimasonyeza kupuma chifukwa choti ganizo latha.
Page 52 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Mpatuliro
Mpatuliro ndi chizindikiro chomwe chimagwiritsidwa ntchito tikafuna kupuma pang’ono pamene
tikutchula mawu omwe ali m’mndandanda.
Kawirikawiri mawu a m’mndandandawo amakhala mayina, alowam’malo ndi afotokozi.
Zitsanzo
a. Mundigulireko nsomba, mchere, anyezi, kale ndi mafuta ophikira.
b. Kumsonkhano kunali Azungu, Amwenye ndi anthu akuda.
c. Mwanayo ndi wamfupi, wakuda, wanzeru, waulemu komanso wosekaseka.
Mpatuliro umagwiranso ntchito yopatula nthambi yosaima payokha ku nthambi yoima payokha.
Zitsanzo
a. Popeza mwandiitana, ndabwera.
b. Ngakhale kunali mvula, iwo anapitabe kuphwando.
c. Chalaka bakha, nkhuku singatole.
Mpatuliro umaikidwanso pambuyo pa mawu omwe ali m’mtengero m’malo mwa mtamuliro.
Zitsanzo
a. Iye adati, “Chakudza sichiyimba ng’oma.”
b. Kodi Yohane anati, “Tikumane poduka mphepo”?
c. “Chabwino,” mayi anayankha, “ndigula nsapatozo.”
Mpatuliro umagwiritsidwanso ntchito polemba keyala yopingasa. Kumapeto kwa mzere uliwonse mu
keyala yopingasa (kupatula mzere wotsiriza) kumakhala mpatuliro.
Page 53 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Chitsanzo
Kambilonjo pulaimale sukulu,
Positi Ofesi 11,
Kaloga,
Ntcheu.
Mpatuliro umagwiritsidwanso ntchito popatula mawu oyankhira (maka aonjezi) ndi mawu otsatira.
Zitsanzo
a. Chabwino, mubwere mawa.
b. Inde, ndi zowona kuti ndimamukonda.
c. Ayi, sindifuna zachipongwe.
3. Mtamuliro
Mtamuliro ndi chizindikiro chomwe nthawi zambiri chimagwiritsidwa ntchito pofuna kutambasula zomwe
zanenedwa kale.
Mtamuliro umatamula (umatchula) mndandanda wa zinthu ndipo umaikidwa patsogolo pa alozi kapena
mawu oti ‘monga’ ndi ‘mwachitsanzo’.
Zitsanzo
a. Mundigulireko zinthu izi: nsapato, malaya ndi mabuku.
b. Iye anapambana maphunziro atatu awa: Chichewa, Chingerezi ndi Chilatini.
c. Unditengereko izi: mpeni, mbale ndi mphika.
Mtamuliro umagwiranso ntchito yotsekula mawu omwe amayankhulidwa mwachindunji ndi munthu wina
ndipo ali m’mtengero.
Zitsanzo
a. Zione anati: “Ndifuna kudzakhala mtsogoleri wa dziko.”
b. Akuluakulu adati: “Ukasowa mn’gona umadya mavu.”
c. Kamuzu adati: “Chuma cha Malawi chili m’nthaka.”
4. Mpumirapang’ono
Mpumirapang’ono umagwira ntchito mu chiganizo cha ziganizo zingapo kapena cha nthambi pofuna
kupuma motalikirako tisanamalize ganizo. Chizindikirochi chili pakati pa mpatuliro ndi mpumiro.
Chizindikirochi chimaikidwa pamalo pamene pakanatha kuikidwa alumikizi monga awa: ‘chifukwa’, ‘poti’,
‘popeza’, ndi ‘kapena’ pofuna kulumikiza nthambi za chiganizo.
Zitsanzo
a. M’mudzimo mulibe anthu; onse anasamukamo.
b. Sindikuperekezani; sindinasambe.
c. Tsogolani; sindifuna kuti andione.
Page 54 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
Tingathe kugwiritsanso ntchito mpumirapang’ono m’chiganizo cha ziganizo chomwe chili ndi ziganizo
zotsutsana maganizo ngati sitifuna kugwiritsa ntchito alumukizi monga ‘koma’ ndi ‘ngakhale’.
Zitsanzo
a. Ndimakonda therere; mayi anga amadana nalo.
b. Bambo amasuta fodya; ine sindimasuta.
c. Iye amandikonda; ine sindimukonda.
Mpumirapang’ono umagwiranso ntchito pofuna kupatula magulu akuluakulu a mawu omwe ali ndi zinthu
zomwe zili m’mndandanda ndipo alekanitsidwa ndi mipatuliro.
Chitsanzo
Tidzagula nthochi, mbatata ndi buledi kuti tidzadye mawa; mapapaya, mpunga ndi nsomba kuti
tidzadye masana; komanso nyama, masikono ndi zakumwa kuti tidzadye ndi kumwa tsiku
laphwandolo.
5. Mfunsiro
Mfunsiro ndi chizindikiro chomwe chimagwira ntchito pofunsa funso lachindunji.
Zitsanzo
a. Ukuti bwanji?
b. Kodi wadya?
c. Wabwera?
6. Mfuwuliro
Ichi ndi chizindikiro chimene chimalembedwa patsogolo pa mawu omwe ayankhulidwa mofuwula kapena
mokuwa pofuna kusonyeza kudzidzimuka, kudabwa, kumva ululu, kusangalala kapena kunyansidwa.
Zitsanzo
a. Hi! Pali njoka.
b. Kalanga ine! Ndavulala.
c. Moto kuno! Motoo!
Page 55 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
7. Nkhodolero
Chizindikirochi chimalembedwa pomwe patsala mpata tikachotsa lembo lina pa mawu, maka lembo
lamtsekulanjira (lembo laliwu).
Zitsanzo
a. m'nyanja (mu nyanja)
b. n’kale (ndi kale)
c. cham’gwera (chamugwera)
Pali maphatikizo ena mu Chichewa omwe amakhala ndi nkhodolero yomwe sisonyeza kuti pachotsedwa
lembo koma kuti maphatikizowo ndi madzeram’mphuno.
Zitsanzo
a. ng’amba
b. ng’ombe
c. ching’wenyeng’wente
Nthawi zina nkhodolero imaikidwa pa mawu pofuna kusiyanitsa mawuwo ndi mawu ena ofanana nawo
m’kalembedwe koma osiyana katchulidwe ndi matanthauzo.
Chitsanzo
mbale ndi m’bale
mbale: chipangizo chodyeramo
m’bale: munthu wobadwa naye bere limodzi kapena banja limodzi
8. Mdulamawu
Chizindikirochi chimagwira ntchito zosiyanasiyana monga zotsatirazi
Zitsanzo
i) Lilongwe (Li-lo-ngwe)
ii) kang’wing’wi (ka-ng’wi-ng’wi)
iii) mphunzitsi (m-phu-nzi-tsi)
b. Kusonyeza aphatikiri
Zitsanzo
i) mphatikiram’mbuyo : ka- (kanthu), a- (apusi), -na- (anadya), -ku- (tikubwera)
ii) mphatikiram’tsogolo : -era (tengera), -ana (kondana), -etsetsa (onetsetsa)
iii) akulitsi : -nso (bweranso), -be (sungabe), -tu (tengatu), -di (munthudi)
Page 56 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
c. Polemba magulu a mayina
Zitsanzo
Mu-, Mi- ; Li-, Ma- ; Ka-, Ti- ; Chi-, Zi-
Kumbutso
Sitigwiritsa ntchito mdulamawu polemba mawu ophatikizana ndi achibwereza.
Zitsanzo
a. njokaluzi (osati njoka-luzi)
b. kawirikawiri (osati kawiri-kawiri)
c. tumphatumpha (osati tumpha-tumpha)
9. Mkutiramawu
Chizindikirochi chimagwira ntchito zotsatirazi:
a. Kupereka mawu ena ofanana tanthauzo ndi omwe akuyang’anidwa mwachindunji.
Zitsanzo
i) Iye wachita kaguni (manyazi) atamuseka.
ii) Galu wanu wapha nkhawena (nkhanga) yanga.
Zitsanzo
i) Lembani ziganizo zomveka bwino ndi zining’a zotsatirazi kuti mukudziwa matanthauzo ake
(chining’a chimodzi pa chiganizo chimodzi).
ii) Nyumbayo ndiyosasowa kwenikweni chifukwa ngakhale mwana amaidziwa. Ngati
mungasokere, mutha kufunsa (koma osafunsa anthu okaikitsa).
Page 57 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
10. Mtengero
Ntchito yaikulu ya chizindikiro chimenecho ndi kukuta zomwe munthu wina wayankhula (zoyankhula
mwini).
Zitsanzo
a. Iye anati, “Kwapsa tonola sudziwa mtima wa moto.”
b. “Ndabwera,” John anandiuza, “kudzaona amayi.”
c. “Kodi mwadya kale?” mnzanga anandifunsa.
Mtengero umagwiritsidwanso ntchito pokuta mitu ya m’buku, ndakatulo, nyimbo, nthano za makolo,
nkhani zazifupi ndi nkhani zazitali.
Zitsanzo
a. Onani mu buku la Mbiri ya Achewa za “Ufumu wa Mkanthama Mwale” pa tsamba 120.
b. Ine sindinawerengeko ndakatulo yotchedwa “Chilola wopanda mano” ndi nkhani yayifupi ya “Zina
ukaona”.
c. Wambali Mkandawire anaimba nyimbo ya “Kujipereka”.
Zitsanzo
a. Ulimi wothirira ndi waphindu.
b. Akuti akupezani posachedwapa.
Page 58 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Poyamba kulemba mayina a mwinimwini.
Zitsanzo
a. Mtsinje wa Shire ndi waukulu.
b. Dziko la Malawi ndi lamtendere.
c. Dzina lake ndi Zikomo Banda.
3. Polemba malonje a kalata timayamba kulemba dzina la amene tikumulembera ndi lembo lalikulu
ngangale dzinalo likhale dzina lopanda mwinimwini.
Zitsanzo
a. Okondedwa Bambo ndi Mayi.
b. Wokondedwa Bwana.
Zitsanzo
a. Iye ndi mnzanga.
b. Mudzi wathu ndi wamtendere.
Page 59 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
2. Kukhala mlumikizi
Zitsanzo
a. Anyamata ndi atsikana akuphunzira.
b. Iwo agula nsomba ndi nyama.
3. Kukhala mperekezi
Zitsanzo
a. Ndabwera ndi mnzanga.
b. Ali ndi ndalama zambiri.
4. Kukhala mvekero
Zitsanzo
a. Mutu wanga uli ndi.
b. Mumange mtolowo kuti ndi.
Page 60 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 17 ZAZIMUNA NDI ZAZIKAZI
Chachimuna Chachikazi
atate amayi
bambo mayi
tatavyala mpongozi
mnyamata mtsikana
boyi puma
gojo/gocho chumba
kapolo mdzakazi
mphulu nkhosa
tsibweni/malume zakhali
chisodzera/muna buthu
mzambwe nkhunda
ndoda ntchembere
nthondo ntchewa/ntchowa
phungu nankungwi
wakunjira
nankungwi
tambala
thadzi
mfule mzindi
chipsolopsolo msoti
mtheno mzinda/mdzidzi
mfumu mfumukazi
mumphwa mfumakazi
mkwati mkwatibwi
mwamuna
mkazi
nkhunzi mthoni
muna mbombe
tonde mkota
bwana dona
mchimwene mchemwali
tambala msoti
mkamwini mtengwa
Page 61 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 18 MAWU OTSUTSANA M’MATANTHAUZO
fatsa chenjera
Page 62 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 19 MAWU OFANANA M’MATANTHAUZO
Page 63 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789
MUTU 20 ZAZIKULU NDI ZAZING’ONO
Chachikulu chaching’ono
bambo mnyamata
galu mphonda/nkhanda
fodya mbande
chule mbululu/mbiriwidzi/mbuludzi/mkulumutu
nkhunda chiunda
nkhuku mwanapiye
ndoda kamuna
ng’ombe msona
MIE (2008), Buku la Ophunzira la Chichewa la Maphunziro a M’sukulu Zauphunzitsi (IPTE), Domasi; MIE
Page 64 of 64
TIFERANJI PHIRI 0884 429 789